Pamenepo Davide anapatsa Solomoni mwana wake chifaniziro cha chipinda cholowera cha Kachisi, ndi cha nyumba zake, ndi cha zosungiramo chuma zake, ndi cha zipinda zosanjikizana zake, ndi cha zipinda zake za m'katimo, ndi cha Kachisi wotetezerepo;
Eksodo 25:40 - Buku Lopatulika Ndipo uyang'anire uzipanga monga mwachifaniziro chao, chimene anakuonetsa m'phirimo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo uyang'anire uzipanga monga mwachifaniziro chao, chimene anakuonetsa m'phirimo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Usamale kuti upange zimenezi monga momwe ndikukuwonetsera paphiri pano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.” |
Pamenepo Davide anapatsa Solomoni mwana wake chifaniziro cha chipinda cholowera cha Kachisi, ndi cha nyumba zake, ndi cha zosungiramo chuma zake, ndi cha zipinda zosanjikizana zake, ndi cha zipinda zake za m'katimo, ndi cha Kachisi wotetezerepo;
Chonsechi, anati Davide, anandidziwitsa ndi kuchilemba kuchokera kwa dzanja la Yehova; ndizo ntchito zonse za chifaniziro ichi.
Ndipo anapanga zoikaponyali khumi zagolide, monga mwa ziweruzo chake; naziika mu Kachisi, zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere.
Monga mwa zonse Ine ndilikuonetsa iwe, chifaniziro cha chihema, ndi chifaniziro cha zipangizo zake zonse, momwemo uchimange.
ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha zonunkhira zokoma za malo opatulika; azichita monga mwa zonse ndakuuza iwe.
Ndipo Mose adaitana Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu onse aluso, amene Yehova adaika luso m'mtima mwao, onse ofulumidwa mtima ayandikize kuntchito kuichita.
Ndipo mapangidwe ake a choikaponyali ndiwo golide wosula; kuyambira tsinde lake kufikira maluwa ake anachisula; monga mwa maonekedwe ake Yehova anaonetsa Mose, momwemo anachipanga choikaponyali.
Chihema cha umboni chinali ndi makolo athu m'chipululu, monga adalamula Iye wakulankhula ndi Mose, achipange ichi monga mwa chithunzicho adachiona.
amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri.
Chifukwa chake tinati, Kudzali, akadzatero kwa ife, kapena kwa mibadwo yathu m'tsogolomo, kuti tidzati, Tapenyani, chitsanzo cha guwa la nsembe la Yehova, chomanga makolo athu, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai, koma ndilo mboni pakati pa ife ndi inu.