Ndipo uzipanga choikaponyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;
Eksodo 25:34 - Buku Lopatulika Ndipo pa choikaponyali chomwe pakhale zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pa choikapo nyali chomwe pakhale zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa choikaponyalecho padzakhale maluŵa anai a maonekedwe onga maluŵa amtowo, okhala ndi nkhunje ndi maluŵa ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa choyikapo nyalecho pakhale zikho zinayi zopangidwa ngati maluwa amtowo ali ndi mphukira ndi maluwa. |
Ndipo uzipanga choikaponyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;
Ndipo pa choikaponyali chomwe panali zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake;
Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.