Eksodo 25:27 - Buku Lopatulika Mphetezo zikhale pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko za kunyamulira nazo gome. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mphetezo zikhale pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko za kunyamulira nazo gome. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mphete zopisamo mphiko zonyamulira tebulolo ziikidwe pafupi ndi fulemu lija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mphetezo uziyike kufupi ndi feremu kuti azikolowekamo nsichi zonyamulira tebuloyo. |
Nulipangire mitanda pozungulirapo yoyesa chikhato m'kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira upangirepo mkombero wagolide.
Nulipangire mphete zinai zagolide, ndi kuika mphetezo pangodya zinai zokhala pa miyendo yake inai.
Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide, kuti anyamulire nazo gome.
Ndipo uzikuta matabwa ndi golide, ndi kupanga mphete zao zagolide zopisamo mitandayo; uzikutanso mitandayo ndi golide.