Ndipo uliyengere mphete zinai zagolide, ndi kuziika kumiyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziwiri pa ina.
Eksodo 25:26 - Buku Lopatulika Nulipangire mphete zinai zagolide, ndi kuika mphetezo pangodya zinai zokhala pa miyendo yake inai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nulipangire mphete zinai zagolide, ndi kuika mphetezo pangodya zinai zokhala pa miyendo yake inai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Upange mphete zinai zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zinai za ku miyendo yake inai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Upange mphete zinayi zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zake zinayi, kumene kuli miyendo yake inayi. |
Ndipo uliyengere mphete zinai zagolide, ndi kuziika kumiyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziwiri pa ina.
Nulipangire mitanda pozungulirapo yoyesa chikhato m'kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira upangirepo mkombero wagolide.