Ndi kuchindikira kwake kunanga chikhato, ndi mlomo wake unasadamuka ngati mlomo wa chomwera, ngati duwa la kakombo; analowamo madzi a mitsuko yaikulu zikwi zitatu.
Eksodo 25:25 - Buku Lopatulika Nulipangire mitanda pozungulirapo yoyesa chikhato m'kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira upangirepo mkombero wagolide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nulipangire mitanda pozungulirapo yoyesa chikhato m'kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira upangirepo mkombero wagolide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Upange fulemu lozungulira tebulo, muufupi mwake kuyesa chikhatho, ndipo upange mkombero wagolide wozungulira fulemulo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Upange feremu yozungulira tebulo, mulifupi mwake ngati chikhatho cha dzanja, ndipo uyike mkombero wagolide kuzungulira feremuyo. |
Ndi kuchindikira kwake kunanga chikhato, ndi mlomo wake unasadamuka ngati mlomo wa chomwera, ngati duwa la kakombo; analowamo madzi a mitsuko yaikulu zikwi zitatu.
Nulipangire mphete zinai zagolide, ndi kuika mphetezo pangodya zinai zokhala pa miyendo yake inai.
Ndipo ulikute ndi golide woona, pamwamba pake ndi mbali zake zozungulira, ndi nyanga zake; ulipangirenso mkombero wagolide pozungulira.
Analipangiranso mitanda pozungulirapo, yoyesa chikhato m'kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira anapangirapo mkombero wagolide.
ndipo analikuta ndi golide woona m'kati ndi kunja, nalipangira mkombero wa golide pozungulira pake.
Ndipo miyeso ya guwa la nsembe, kuyesa mikono ndi iyi: (mkonowo ndiwo mkono ndi chikhato), tsinde lake likhale mkono, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi, ndi mkuzi wake m'mphepete mwake pozungulira pake kuyesa zala; ili ndi tsinde la guwali.