Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 25:23 - Buku Lopatulika

Ndipo uzipanga gome la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo uzipanga gome la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Upange tebulo la matabwa a mtengo wa kasiya, kutalika kwake masentimita 91, muufupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Upange tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69.

Onani mutuwo



Eksodo 25:23
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anapanga zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova: guwa la nsembe lagolide, ndi gome lagolide loikapo mikate yoonekera;


ndi zoikaponyali za golide woyengetsa, zisanu ku dzanja lamanja, zisanu kulamanzere, chakuno cha chipinda chamkati, ndi maluwa ndi nyali ndi mbano zagolide;


ndi golide woyesedwa kulemera kwake wa magome a mkate woonekera, wa gome lililonse; ndi siliva wa magome asiliva,


Solomoni anapanganso zipangizo zonse zinali m'nyumba ya Mulungu, guwa la nsembe lagolide lomwe, ndi magome oikapo mkate woonekera;


Anapanganso magome khumi, nawaika mu Kachisi, asanu ku dzanja lamanja, ndi asanu ku dzanja lamanzere. Napanga mbale zowazira zana limodzi zagolide.


ndi gomelo ndi zipangizo zake, ndi choikaponyali choona ndi zipangizo zake, ndi guwa la nsembe lofukizapo;


gome, ndi mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkate woonekera;


Guwa la nsembe linali lamtengo, msinkhu wake mikono itatu, ndi m'litali mwake mikono iwiri, ndi ngodya zake, ndi tsinde lake, ndi thupi, nza mtengo; ndipo ananena ndi ine, Ili ndiko gome lili pamaso pa Yehova.


Ndipo utiike m'mizere iwiri, tisanu ndi kamodzi mzere umodzi, pa gome loyera, pamaso pa Yehova.


Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikaponyali, ndi maguwa a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.


Ndipo ayale pa izi nsalu yofiira, ndi kuliphimba ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.


Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m'menemo munali choikaponyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika.