Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwake.
Eksodo 25:22 - Buku Lopatulika Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndili pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndili pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndizidzakumana nawe kumeneko, ndipo kuchokera pamwamba pa chivundikirocho, pakati pa akerubi ali pamwamba pa bokosiwo, ndidzakuuza malamulo okhudza anthu anga Aisraele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndizidzakumana nawe pamenepo, pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo, pakati pa Akerubi awiriwo, ndikumadzakupatsa malamulo onse okhudzana ndi Aisraeli. |
Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwake.
Ndipo Davide ananyamuka, namuka nao anthu onse anali naye, nachokera ku Baale-Yuda natengako likasa la Mulungu, limene amatchula nalo Dzinalo, Dzina la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa Akerubi.
Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati, Yehova Mulungu wa Israele wakukhala pakati pa akerubi, Inu ndinu Mulungu mwini wake, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Ndipo Davide ndi Aisraele onse pamodzi naye anakwera kunka ku Baala, ndiko ku Kiriyati-Yearimu wa mu Yuda, kukwera nalo kuchokera komweko likasa la Mulungu Yehova wakukhala pa akerubi, kumene aitanirako Dzina.
Mbusa wa Israele, tcherani khutu; inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; inu wokhala pa akerubi, walitsani.
Utsani chamuna chanu pamaso pa Efuremu ndi Benjamini ndi Manase, ndipo mutidzere kutipulumutsa.
Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere; Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.
Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.
Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.
nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m'chihema chokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uchiyese chopatulika ndithu.
Nuliike chakuno cha nsalu yotchinga ili ku likasa la mboni, patsogolo pa chotetezerapo chili pamwamba pa mboni, pomwe ndidzakomana ndi iwe.
Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, paphiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.
Ndipo Ine, taona, ndampatsa Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, akhale naye; ndipo ndaika luso m'mitima ya onse a mtima waluso, kuti apange zonse ndakuuza iwe;
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, amene mukhala pa akerubi, Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.
Ndipo polowa Mose ku chihema chokomanako, kunena ndi Iye, anamva mau akunena naye ochokera ku chotetezerapo chili pa likasa la mboni, ochokera pakati pa akerubi awiriwo; ndipo Iye ananena naye.
Ndipo ana a Israele anafunsira kwa Yehova; pakuti likasa la chipangano la Mulungu linakhala komweko masiku aja,
Chifukwa chake anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la chipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa akerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Finehasi anali komweko ndi likasa la chipangano la Mulungu.