Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.
Eksodo 25:18 - Buku Lopatulika Uzipanganso akerubi awiri agolide; uwasule mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Uzipanganso akerubi awiri agolide; uwasule mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa mbali ziŵiri za chivundikirocho, m'mphepete mwake, upange akerubi aŵiri, agolide, osula ndi nyundo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo upange Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo, uwayike mbali ziwiri za chivundikirocho, |
Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.
ndi cha guwa la nsembe lofukizapo la golide woyengetsa woyesedwa kulemera kwake, ndi chifaniziro cha galeta wa akerubi agolide akufunyulula mapiko ao ndi kuphimba likasa la chipangano la Yehova.
Ndipo m'malo opatulika kwambiri anapanga akerubi awiri, anachita osema, nawakuta ndi golide.
Ndipo uzipanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu.
Nupange kerubi mmodzi ku thungo lino, ndi kerubi wina ku thungo lina; upange akerubi ochokera kuchotetezerapo, pa mathungo ake awiri.
Mitu yao ndi mphanda zao zikhale zotuluka m'mwemo; chonsechi chikhale chosulika chimodzi cha golide woona.
Ndipo Yehova analankhula ndi munthu wovala bafuta, nati, Lowa pakati pa njingazi pansi pa kerubi, nudzaze manja ako makala a moto ochokera pakati pa akerubi, nuwamwaze pamwamba pa mzinda. Nalowa, ndili chipenyere ine.
Awa ndi zamoyozo ndinaziona pansi pa Mulungu wa Israele kumtsinje Kebara, ndipo ndinadziwa kuti ndiwo akerubi.
Tsono akerubi anaima kudzanja lamanja la nyumba polowa munthuyo, ndi mtambo unadzaza bwalo la m'kati.
ndi pamwamba pake akerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitingathe kunena tsopano paderapadera.
Chifukwa chake anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la chipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa akerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Finehasi anali komweko ndi likasa la chipangano la Mulungu.