Pamenepo Davide anapatsa Solomoni mwana wake chifaniziro cha chipinda cholowera cha Kachisi, ndi cha nyumba zake, ndi cha zosungiramo chuma zake, ndi cha zipinda zosanjikizana zake, ndi cha zipinda zake za m'katimo, ndi cha Kachisi wotetezerepo;
Eksodo 25:17 - Buku Lopatulika Ndipo uzipanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo uzipanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Upange ndi golide wabwino kwambiri chivundikiro cha bokosi, kutalika kwake masentimita 114, kupingasa kwake masentimita 69. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Upange chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. |
Pamenepo Davide anapatsa Solomoni mwana wake chifaniziro cha chipinda cholowera cha Kachisi, ndi cha nyumba zake, ndi cha zosungiramo chuma zake, ndi cha zipinda zosanjikizana zake, ndi cha zipinda zake za m'katimo, ndi cha Kachisi wotetezerepo;
Uzipanganso akerubi awiri agolide; uwasule mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo.
Ndipo anapanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu.
Ndipo anatenga mboniyo, naiika m'likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa;
Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali paphiri lopatulika la Mulungu, anayendayenda pakati pa miyala yamoto.
amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m'mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m'kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe;
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.
ndi pamwamba pake akerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitingathe kunena tsopano paderapadera.
ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.