Ndipo ana a Alevi anasenza likasa la Mulungu pa mapewa ao, mphiko zili m'mwemo, monga Mose anawauza, monga mwa mau a Yehova.
Eksodo 25:14 - Buku Lopatulika Nupise mphiko m'mphetezo pa mbali zake za likasa, zakunyamulira nazo likasalo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nupise mphiko m'mphetezo pa mbali zake za likasa, zakunyamulira nazo likasalo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mphiko zimenezo udzazilonge m'mphetezo pa mbali ziŵiri za bokosilo, kuti azinyamulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ulowetse nsichizo mʼmphete zija za mbali zonse ziwiri za bokosilo kuti azinyamulira. |
Ndipo ana a Alevi anasenza likasa la Mulungu pa mapewa ao, mphiko zili m'mwemo, monga Mose anawauza, monga mwa mau a Yehova.
Pamenepo Davide anati, Sayenera ena kusenza likasa la Mulungu koma Alevi ndiwo; pakuti Yehova anawasankha iwo kusenza likasa la Mulungu, ndi kumtumikira Iye kosatha.
Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide, kuti anyamulire nazo gome.
Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake; uziike pa nthiti zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo.
Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe, nanena nao, Senzani likasa la chipangano, ndi ansembe asanu ndi awiri anyamule mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, kutsogolera nazo likasa la Yehova.