Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 25:13 - Buku Lopatulika

Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Upangenso mphiko zakasiya, ndipo mphikozo uzikute ndi golide.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kenaka upange mizati yamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide.

Onani mutuwo



Eksodo 25:13
14 Mawu Ofanana  

Ndipo mphikozo zinatalika kuti nsonga za mphiko zidaoneka ku malo opatulika chakuno cha chipinda chamkati; koma sizinaoneke kubwalo; ndipo zikhala pomwepo mpaka lero lino.


Ndipo ana a Alevi anasenza likasa la Mulungu pa mapewa ao, mphiko zili m'mwemo, monga Mose anawauza, monga mwa mau a Yehova.


Ndipo uliyengere mphete zinai zagolide, ndi kuziika kumiyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziwiri pa ina.


Nupise mphiko m'mphetezo pa mbali zake za likasa, zakunyamulira nazo likasalo.


Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide, kuti anyamulire nazo gome.


ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;


Ndipo upangire guwa la nsembe mphiko, mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi mkuwa.


Ndipo upange mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide.


Ndipo anapanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi golide.


Ndipo anatenga mboniyo, naiika m'likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa;


Ndipo paguwa la nsembe lagolide aziyala nsalu ya madzi, naliphimbe ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.


Naikepo zipangizo zake zonse, zimene atumikira nazo pamenepo, mbale za zofukiza, mitungo, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, zipangizo zonse za guwa la nsembe; nayalepo chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.


ndi kuikapo chophimba cha zikopa za akatumbu; ndi kuyalapo nsalu yamadzi yeniyeni, ndi kupisako mphiko zake.


Ndipo ayale pa izi nsalu yofiira, ndi kuliphimba ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.