Ndi chipinda cholowera chinali kukhomo kwa nyumba, m'litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba munali mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake zana limodzi mphambu makumi awiri; ndipo analikuta m'katimo ndi golide woona.
okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaaphukayo, ndi magome a chipangano;