Eksodo 23:28 - Buku Lopatulika Ndipo ndidzatumiza mavu akutsogolere amene adzaingitsa Ahivi, Akanani, ndi Ahiti, pamaso pako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndidzatumiza mavu akutsogolere amene adzaingitsa Ahivi, Akanani, ndi Ahiti, pamaso pako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzapirikitsa Ahivi, Akanani ndi Ahiti, inu musanafike, ndipo adzathaŵa monga ngati ndaŵatumira mavu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ahivi, Akanaani ndi Ahiti adzathawa ngati kuti ndawatumizira mavu. |
ndipo ndidzatuma mthenga akutsogolere; ndipo ndidzapirikitsa Akanani, ndi Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;
Dzisungire chimene Ine ndikuuza lero lino: taona, ndiingitsa pamaso pako Aamori ndi Akanani, ndi Ahiti ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.
Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.
Komanso Yehova Mulungu wanu adzatumiza mavu pakati pao, kufikira ataonongeka otsalawo, ndi akubisala pamaso panu.