Eksodo 22:26 - Buku Lopatulika Ukati ulandire chikole kaya chovala cha mnansi wako, koma polowa dzuwa uchibwezere kwa iye; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ukati ulandire chikole kaya chovala cha mnansi wako, koma polowa dzuwa uchibwezere kwa iye; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mukatenga mwinjiro wa munthu wina ngati chigwiriro kuti adzakulipireni, muubweze dzuŵa lisanaloŵe, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mukatenga chovala cha mnzanu kuti chikhale chikole mumubwezere dzuwa lisanalowe |
Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.
Tenga malaya a woperekera mlendo chikole; woperekera mkazi wachilendo chikole umgwire mwini.
kapena kusautsa wina aliyense, wosatenga chigwiriro, wosatenga zofunkha; koma anapatsa wanjala chakudya chake, naveka wamaliseche ndi chovala,
wosasautsa munthu aliyense, koma wambwezera wangongole chigwiriro chake, wosatenga zofunkha, anampatsa wanjala chakudya chake, naveka wamaliseche ndi chovala,
woipayo akabweza chikole, nakabweza icho anachilanda mwachifwamba, nakayenda m'malemba a moyo wosachita chosalungama, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.
nagona pansi pa zofunda za chikole kumaguwa a nsembe ali onse, ndi m'nyumba ya Mulungu wao akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa.
Musamaipsa mlandu wa mlendo, kapena wa ana amasiye; kapena kutenga chikole chovala cha mkazi wamasiye;
Munthu asalandire chikole mphero, ngakhale mwanamphero, popeza alandirapo chikole moyo wa munthu.