Eksodo 21:35 - Buku Lopatulika Ng'ombe ya mwini ikapweteka ng'ombe ya mnzake, nifa, azigulitsa ng'ombe yamoyoyo, nagawe ndalama zake; naigawe, ndi yakufa yomweyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ng'ombe ya mwini ikapweteka ng'ombe ya mnzake, nifa, azigulitsa ng'ombe yamoyoyo, nagawe ndalama zake; naigawe, ndi yakufa yomweyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ng'ombe ya munthu wina ikapha ng'ombe ya mnzake, anthu aŵiriwo agulitse ng'ombe yamoyoyo, ndipo ndalama zake agaŵane. Nyama yake ya ng'ombe yakufayo agaŵanenso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ngati ngʼombe ya munthu wina ipha ngʼombe ya mnzake, ngʼombe yamoyo ija igulitsidwe ndipo anthu awiriwo agawane pakati ndalama yake. Achite chimodzimodzi ndi ngʼombe yakufa ija. |
Kapena kudadziwika kuti ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yake.