Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kuphwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amtchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza.
Eksodo 21:30 - Buku Lopatulika Akamuikira dipo, azipereka chiombolo cha moyo wake monga mwa zonse adamuikira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akamuikira dipo, azipereka chiombolo cha moyo wake monga mwa zonse adamuikira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ngati amlamula kuti adziwombole, adzayenera kulipira ndalama, kuti apulumutse moyo wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngati wauzidwa kuti alipire, iye apereke zimene wauzidwazo kuti awombole moyo wake. |
Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kuphwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amtchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza.
Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso.
Pamene uwerenga ana a Israele, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.