Ndipo akagulula dzino la mnyamata wake, kapena dzino la mdzakazi wake, azimlola amuke waufulu chifukwa cha dzino lake.
Eksodo 21:28 - Buku Lopatulika Ng'ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng'ombeyo, osadya nyama yake; koma mwini ng'ombeyo azimasuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ng'ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng'ombeyo, osadya nyama yake; koma mwini ng'ombeyo azimasuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ng'ombe ikapha munthu wamwamuna kapena wamkazi ndi nyanga, iponyedwe miyala, ndipo nyama yake musadye. Koma mwiniwake wa ng'ombeyo asalangidwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ngati ngʼombe ipha munthu wamwamuna kapena wamkazi ndi nyanga yake, iponyedwe miyala ndipo nyama yake isadyedwe. Ndipo mwini ngʼombeyo asayimbidwe mlandu. |
Ndipo akagulula dzino la mnyamata wake, kapena dzino la mdzakazi wake, azimlola amuke waufulu chifukwa cha dzino lake.
Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso.
Ng'ombeyo ikatunga mnyamata kapena mdzakazi, azipatsa mbuye wake ndalama za masekeli a siliva makumi atatu, ndipo ng'ombeyo aiponye miyala.