Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Eksodo 21:17 - Buku Lopatulika Munthu wakutemberera atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munthu wakutemberera atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Munthu aliyense wotemberera bambo wake kapena mai wake, aphedwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa. |
Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Akalimbana amuna, ndipo wina akakantha mnzake ndi mwala, kapena ndi nkhonya, wosafa iye, koma wakhulungira pakama;
Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.
Munthu akakhala naye mwana wamwamuna wopulukira, ndi wopikisana naye, wosamvera mau a atate wake, kapena mau a mai wake, wosawamvera angakhale anamlanga;
Pamenepo amuna onse a mzinda wake amponye miyala kuti afe; chotero muchotse choipacho pakati panu; ndipo Israele wonse adzamva, nadzaopa.