Pamenepo Sekaniya mwana wa Yehiyele, mwana wina wa Elamu, anambwezera Ezara mau, nati, Talakwira Mulungu wathu, tadzitengera akazi achilendo a mitundu ya dzikoli; koma tsopano chimtsalira Israele chiyembekezo kunena za chinthu ichi.
Eksodo 18:24 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anamvera mau a mpongozi wake, nachita zonse adazinena. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anamvera mau a mpongozi wake, nachita zonse adazinena. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adamvera zonse zimene adanena Yetero zija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anamvera mpongozi wake ndi kuchita zonse zimene iye ananena. |
Pamenepo Sekaniya mwana wa Yehiyele, mwana wina wa Elamu, anambwezera Ezara mau, nati, Talakwira Mulungu wathu, tadzitengera akazi achilendo a mitundu ya dzikoli; koma tsopano chimtsalira Israele chiyembekezo kunena za chinthu ichi.
Nanyamuka Ezara, nalumbiritsa akulu a ansembe, ndi Alevi, ndi Aisraele onse, kuti adzachita monga mwa mau awa. Nalumbira iwo.
Tamvera mau anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m'malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo milandu kwa Mulungu;
Ukachite chinthuchi, ndi Mulungu akakuuza chotero, udzakhoza kupirira, ndi anthu awa onse adzapita kwao mumtendere.
Ndipo Mose anasankha amuna anzeru mwa Aisraele onse, nawaika akulu a pa anthu, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, ndi akulu a pa makumi.
Ndipo diso silingathe kunena kwa dzanja, Sindikufuna iwe, kapenanso mutu kwa mapazi, Sindikufunani inu.