Ndipo Mose anati, Awa ndi mau anauza Yehova, Dzazani omeri nao, asungikire mibadwo yanu; kuti aone mkatewo ndinakudyetsani nao m'chipululu, muja ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito.
Eksodo 16:33 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mphika, nuthiremo mana odzala omeri, nuuike pamaso pa Yehova, usungikire mibadwo yanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mphika, nuthiremo mana odzala omeri, nuuike pamaso pa Yehova, usungikire mibadwo yanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Mose adauza Aroni kuti, “Tenga mtsuko, uikemo mana wokwana malita aŵiri. Utatero uike pamaso pa Chauta kuti manayo asungike chifukwa cha zidzukulu zanu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Mose anati kwa Aaroni, “Tenga mtsuko ndipo uyikemo malita awiri a mana. Ndipo uyike manawo pamaso pa Yehova kusungira mibado imene ikubwera.” |
Ndipo Mose anati, Awa ndi mau anauza Yehova, Dzazani omeri nao, asungikire mibadwo yanu; kuti aone mkatewo ndinakudyetsani nao m'chipululu, muja ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito.
okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaaphukayo, ndi magome a chipangano;
Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wopambana, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pamwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.