Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe.
Eksodo 16:27 - Buku Lopatulika Ndipo kunali tsiku la Sabata, kuti anthu ena anatuluka kukaola, koma sanaupeze. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali tsiku la Sabata, kuti anthu ena anatuluka kukaola, koma sanaupeze. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo anthu ena adaapita kuti akatole chakudya, koma sadachipeze. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Komabe anthu ena anapita kuti akatole chakudya tsiku lachisanu ndi chiwiri, koma sanapeze kanthu. |
Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Mukana kusunga zouza zanga ndi malamulo anga kufikira liti?