Eksodo 16:20 - Buku Lopatulika Koma sanammvere Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m'mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma sanammvere Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m'mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe ena mwa iwowo sadamvere zimene adaanena Mosezo, adasungako mpaka m'maŵa mwake. Koma kutacha, adaona kuti tonseto tagwa mphutsi, ndipo tikununkha. Apo Mose adaŵapsera mtima anthuwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Komabe ena sanamvere Mose, anasungako mpaka mmawa. Koma mmawa mwake tonse tinali mphutsi zokhazokha. Kotero Mose anawapsera mtima. |
Ndipo anauola m'mawa ndi m'mawa, yense monga mwa njala yake; popeza likatentha dzuwa umasungunuka.
Ndipo anausunga kufikira m'mawa, monga adalamulira Mose; koma sunanunkhe, ndipo sunagwe mphutsi.
Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalande bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa.
Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba:
Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.
Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.
Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha mu Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.