Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwake.
Eksodo 16:17 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Israele anatero, naola wina wambiri, wina pang'ono. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Israele anatero, naola wina wambiri, wina pang'ono. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aisraele adachitadi zimenezo. Ena adatola tambiri, koma ena pang'ono. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aisraeli anachita zonse anawawuza. Ena anatola zambiri ena zochepa. |
Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwake.
Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalire, ndi iye amene adaola pang'ono sunamsowe; yense anaola monga mwa njala yake.