Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akuvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.
Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.
Ndipo pamene anafuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aejipito nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya chochita Ine mu Ejipito; ndipo munakhala m'chipululu masiku ambiri.