Ndipo Eliya anagwira chofunda chake, nachipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.
Eksodo 14:29 - Buku Lopatulika Koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi lamanzere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi lamanzere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Aisraele onse aja adaoloka nyanjayo pansi pali pouma, madzi atangoima pa mbali zonse ziŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Aisraeli aja anawoloka nyanja pansi pali powuma, madzi atachita khoma kumanja ndi kumanzere kwawo. |
Ndipo Eliya anagwira chofunda chake, nachipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.
Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.
Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inaphwa: Potero anawayendetsa mozama ngati m'chipululu.
Ndipo ana a Israele analowa pakati pa nyanja pouma; ndi madziwo anakhala kwa iwo ngati khoma palamanja, ndi palamanzere.
Pakuti akavalo a Farao analowa m'nyanja, ndi magaleta ake ndi apakavalo ake, ndipo Yehova anawabwezera madzi a m'nyanja; koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja.
Ndipo ndi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika, mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu; zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.
Ndipo Yehova adzaononga ndithu bondo la nyanja ya Ejipito; ndipo ndi mphepo yake yopsereza adzagwedeza dzanja lake pa Mtsinje, ndipo adzaimenya ikhale mphaluka zisanu ndi ziwiri, nadzaolotsa anthu pansi pouma.
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Kodi si ndiwe amene unaumitsa nyanja, madzi akuya kwambiri; anasandutsa nyanja zikhale njira ya kupitapo oomboledwa?
waiwala Yehova Mlengi wako, amene anayala m'mwamba, nakhazika maziko a dziko lapansi, ndi kuopabe tsiku lonse chifukwa cha ukali wa wotsendereza, pamene iye akonzeratu kupasula? Uli kuti ukali wa wotsendereza?
Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;
pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mzinda wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.