Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 14:15 - Buku Lopatulika

Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ufuuliranji kwa Ine? Lankhula ndi ana a Israele kuti aziyenda.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ufuuliranji kwa Ine? Lankhula ndi ana a Israele kuti aziyenda.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Apo Chauta adafunsa Mose kuti, “Chifukwa chiyani ukulira kwa ine? Auze Aisraele kuti aziyenda.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Chifukwa chiyani ukufuwulira kwa ine? Uwuze Aisraeli aziyenda.

Onani mutuwo



Eksodo 14:15
9 Mawu Ofanana  

koma Yehova amene anakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lotambasuka, Iyeyu muzimuopa, ndi Iyeyu muzimgwadira, ndi Iyeyu muzimphera nsembe;


Kudatero, popeza ana a Israele adachimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwatulutsa m'dziko la Ejipito pansi padzanja la Farao mfumu ya Aejipito, ndipo anaopa milungu ina,


Nafuulira kwa Yehova Yesaya mneneriyo, nabweza Iye mthunzi m'mbuyo makwerero khumi, ndiwo amene udatsikira pa makwerero a Ahazi.


Ndipo munapenya msauko wa makolo athu mu Ejipito, nimunamva kufuula kwao ku Nyanja Yofiira,


Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete.


Ndipo iwe nyamula ndodo yako, nutambasulire dzanja lako kunyanja, nuigawe, kuti ana a Israele alowe pakati pa nyanja pouma.


Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? Atsala pang'ono kundiponya miyala.


Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako chotere?