Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
Eksodo 12:33 - Buku Lopatulika Ndipo Aejipito anaumiriza anthuwo, nafulumira kuwatulutsa m'dziko; pakuti anati, Tili akufa tonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aejipito anaumiriza anthuwo, nafulumira kuwatulutsa m'dziko; pakuti anati, Tili akufa tonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aejipito adafulumizitsa anthu kuti achoke m'dzikomo, namanena kuti, “Tifatu tonsefe.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aigupto anawawumiriza anthuwo kuti atuluke mofulumira ndi kusiya dziko lawo. Iwo anati, “Ngati sitiwalola kutero, tonse tidzafa.” |
Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
Ndipo anyamata ake a Farao ananena naye, Ameneyo amatichitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Ejipito laonongeka?
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Watsala mliri umodzi ndidzamtengera Farao, ndi Ejipito; pambuyo pake adzakulolani muchoke kuno; pamene akulolani kupita, zoonadi adzakuingitsani kuno konse.
Ndipo anaotcha timitanda topanda chotupitsa ta mtanda umene anabwera nao ku Ejipito, popeza sadaikamo chotupitsa; pakuti adawapirikitsa ku Ejipito, ndipo sanathe kuchedwa, kapena kudzikonzeratu kamba.
Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lake.
Pakuti simudzachoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israele adzadikira pambuyo panu.
Motero, popeza mau a mfumu anafulumiza, ndi ng'anjo inatentha koposa, lawi la moto linapha iwo aja ananyamula Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego.