Ndipo polingirirapo ine, taonani, wadza tonde wochokera kumadzulo, pa nkhope ya dziko lonse lapansi, wosakhudza nthaka; ndi mbuziyo inali ndi nyanga yooneka bwino pakati pamaso ake.
Danieli 8:6 - Buku Lopatulika Ndipo anadzera nkhosa yamphongoyo yokhala ndi nyanga ziwiri, imene ndidaiona ilikuima kumtsinje, naithamangira ndi mphamvu yake yaukali. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anadzera nkhosa yamphongoyo yokhala ndi nyanga ziwiri, imene ndidaiona ilikuima kumtsinje, naithamangira ndi mphamvu yake yaukali. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inabwera molunjika nkhosa yayimuna ya nyanga ziwiri ija imene ndinaona itayima pafupi ndi mtsinje. Ndipo inayithamangira mwaukali. |
Ndipo polingirirapo ine, taonani, wadza tonde wochokera kumadzulo, pa nkhope ya dziko lonse lapansi, wosakhudza nthaka; ndi mbuziyo inali ndi nyanga yooneka bwino pakati pamaso ake.
Ndipo ndinamuona wayandikira pafupi pa nkhosa yamphongo, nawawidwa mtima nayo, naigunda nkhosa yamphongo, nathyola nyanga zake ziwiri; ndipo mphongoyo inalibe mphamvu yakuima pamaso pake, koma anaigwetsa pansi, naipondereza; ndipo panalibe wakupulumutsa mphongoyo m'dzanja lake.