Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi mfumu ya Persiya, kuti abukitse mau mu ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti,
Danieli 6:28 - Buku Lopatulika Momwemo Daniele amene anakuzikabe pokhala Dariusi mfumu, ndi pokhala mfumu Kirusi wa ku Persiya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Momwemo Daniele amene anakuzikabe pokhala Dariusi mfumu, ndi pokhala mfumu Kirusi wa ku Persiya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Danieli anapeza ufulu pa nthawi ya ulamuliro wa Dariyo ndi ulamuliro wa Koresi wa ku Perisiya. |
Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi mfumu ya Persiya, kuti abukitse mau mu ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti,
Atero Kirusi mfumu ya Persiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a padziko lapansi nandilangiza ndimmangire nyumba mu Yerusalemu, ndiwo ku Yuda. Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Yehova Mulungu wake akhale naye, akwereko.
ndi kunena za Kirusi, Iye ndiye mbusa wanga, ndipo adzachita zofuna zanga zonse; ndi kunena za Yerusalemu, Adzamangidwa; ndi kwa Kachisi, Maziko ako adzaikidwa.
amene munaika zizindikiro ndi zodabwitsa m'dziko la Ejipito, mpaka lero lomwe, mu Israele ndi mwa anthu ena; nimunadzitengera mbiri, monga lero lomwe;
Chaka chachitatu cha Kirusi mfumu ya Persiya, chinavumbulutsidwa chinthu kwa Daniele, amene anamutcha Belitesazara; ndipo chinthucho nchoona, ndicho nkhondo yaikulu; ndipo anazindikira chinthucho, nadziwa masomphenyawo.
Chifukwa chake ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uliwonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, adzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.