Ndipo mfumu Nebukadinezara inatumiza kukasonkhanitsa akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, abwere kuzulula fanoli adaliimika mfumu Nebukadinezara.
Danieli 3:3 - Buku Lopatulika Pamenepo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, anasonkhanira kupereka fano adaliimika mfumu Nebukadinezara, naimirira pamaso pa fano adaliimika Nebukadinezara. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, anasonkhanira kupereka fano adaliimika mfumu Nebukadinezara, naimirira pamaso pa fano adaliimika Nebukadinezara. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa, ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, anasonkhana kudzachita mwambo wotsekulira fano limene mfumu Nebukadinezara analiyimika, ndipo mlaliki anayimirira pamaso pa fanolo nati: |
Ndipo mfumu Nebukadinezara inatumiza kukasonkhanitsa akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, abwere kuzulula fanoli adaliimika mfumu Nebukadinezara.
Ndipo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, ndi mandoda a mfumu, atasonkhana, anaona amuna awa, kuti moto unalibe mphamvu pa matupi ao, losawauka tsitsi la pamutu pao, ndi zofunda zao zosasandulika, fungo lomwe lamoto losawaomba.
Ndipo wolalikira anafuulitsa, kuti, Akulamulirani inu anthu, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana,
Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kuchita za m'mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu.