Tsiku lomwelo pakamwa pako padzatsegukira wopulumukayo; mudzalankhula osakhalanso chete, momwemo udzawakhalira chizindikiro; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Danieli 10:15 - Buku Lopatulika Ndipo atanena ndi ine monga mwa mau awa, ndinaweramitsa nkhope yanga pansi ndi kukhala duu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo atanena ndi ine monga mwa mau awa, ndinaweramitsa nkhope yanga pansi ndi kukhala duu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawi yomwe ankanena izi kwa ine, ndinazolika nkhope yanga pansi kusowa chonena. |
Tsiku lomwelo pakamwa pako padzatsegukira wopulumukayo; mudzalankhula osakhalanso chete, momwemo udzawakhalira chizindikiro; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
ndipo ndidzamamatiritsa lilime lako kumalakalaka ako, kuti ukhale wosanena, wosawakhalira wakuwadzudzula; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.
Koma dzanja la Yehova linandikhalira madzulo, asanandifike wopulumukayo; ndipo ananditsegula pakamwa mpaka anandifika m'mawa, m'mwemo panatseguka pakamwa panga, wosakhalanso wosalankhula.
Ndipo ndinamva kunena kwa mau ake, ndipo pamene ndinamva kunena kwa mau ake ndinagwidwa ndi tulo tatikulu pankhope panga, nkhope yanga pansi.
Ndipo m'mene analikulankhula ndi ine ndinagwidwa ndi tulo tatikulu, nkhope yanga pansi; koma anandikhudza, nandiimiritsa pokhala inepo.
Ndipo taona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzachitika izi, popeza kuti sunakhulupirire mau anga, amene adzakwanitsidwa pa nyengo yake.