Nachoka naye Yehoyakini kunka naye ku Babiloni, ndi make wa mfumu, ndi akazi a mfumu, ndi adindo ake, ndi omveka a m'dziko; anachoka nao andende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni.
Danieli 1:3 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu inauza Asipenazi mkulu wa adindo kuti abwere nao ena a ana a Israele, a mbeu ya mafumu, ndi ya akalonga; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu inauza Asipenazi mkulu wa adindo kuti abwere nao ena a ana a Israele, a mbeu ya mafumu, ndi ya akalonga; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono mfumu inalamula Asipenazi, mkulu wa nduna zake kuti abwere nawo ena mwa Aisraeli ochokera mʼbanja laufumu ndi la olemekezeka, |
Nachoka naye Yehoyakini kunka naye ku Babiloni, ndi make wa mfumu, ndi akazi a mfumu, ndi adindo ake, ndi omveka a m'dziko; anachoka nao andende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni.
Taona, masiku afika, kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zimene atate wako anazikundika kufikira lero lino, zidzatengedwa kunka ku Babiloni; sipadzatsala kanthu, ati Yehova.
Ndipo ana ako amene adzabadwa ndi iwe, amene udzabala, iwo adzawatenga, ndipo adzakhala adindo m'chinyumba chake cha mfumu ya ku Babiloni.
Ndipo panali mwezi wachisanu ndi chiwiri, Ismaele mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa mbeu ya mfumu, ndi kapitao wamkulu wa mfumu, ndi anthu khumi pamodzi ndi iye, anadza kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa; pamenepo anadya pamodzi mu Mizipa.