Ndipo pamene ndayang'ana, palibe munthu; ngakhale mwa iwo, palibe phungu, amene angathe kuyankha mau, pamene ndiwafunsa.
Chivumbulutso 5:3 - Buku Lopatulika Ndipo sanathe mmodzi mu Mwamba, kapena padziko, kapena pansi padziko kutsegula pabukupo, kapena kulipenya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo sanathe mmodzi m'Mwamba, kapena padziko, kapena pansi pa dziko kutsegula pabukupo, kapena kulipenya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma panalibe ndi mmodzi yemwe Kumwamba, kapena pa dziko lapansi, kapena kunsi kwa dziko, wotha kufutukula bukulo kapena kuyang'anamo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma panalibe ndi mmodzi yemwe kumwamba kapena pa dziko lapansi kapena kunsi kwa dziko lapansi woti afutukule bukulo kapena kuona zamʼkati mwake. |
Ndipo pamene ndayang'ana, palibe munthu; ngakhale mwa iwo, palibe phungu, amene angathe kuyankha mau, pamene ndiwafunsa.
kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko,
Ndipo cholengedwa chilichonse chili m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi padziko, ndi m'nyanja, ndi zonse zili momwemo, ndinazimva zilikunena, Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi mphamvu, kufikira nthawi za nthawi.
Ndipo ndinalira kwambiri, chifukwa sanapezeke mmodzi woyenera kutsegula bukulo, kapena kulipenya;