Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Chivumbulutso 4:3 - Buku Lopatulika

ndipo maonekedwe a Iye wokhalapo anafanana ndi mwala wa jaspi, ndi sardiyo; ndipo panali utawaleza wozinga mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati smaragido.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndipo maonekedwe a Iye wokhalapo anafanana ndi mwala wa jaspi, ndi sardiyo; ndipo panali utawaleza wozinga mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati smaragido.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Amene adaakhala pampandoyo, maonekedwe ake anali oŵala ngati miyala yoyera ndi yofiira, yonyezimira. Pozungulira mpando wachifumuwo panali utawaleza, maonekedwe ake ngati mwala woŵala, wobiriŵira.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo amene anakhalapoyo anali wa maonekedwe ngati miyala ya jasipa ndi sardiyo. Utawaleza wooneka ngati simaragido unazinga mpando waufumuwo.

Onani mutuwo



Chivumbulutso 4:3
13 Mawu Ofanana  

ndipo anapenya Mulungu wa Israele; ndipo pansi pa mapazi ake panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiro, ndi ngati thupi la thambo loti mbee.


ndi mzere wachiwiri wa nofeki, safiro, ndi yahaloni;


Ndi mzere wachiwiri wa nofeki, safiro, ndi yahalomu.


Chaka chimene mfumu Uziya anafa, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando wachifumu wautali, ndi wotukulidwa, ndi zovala zake zinadzala mu Kachisi.


Ndi pamwamba pathambolo linali pamitu pao panali chifaniziro cha mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati mwala wa safiro; ndipo pa chifaniziro cha mpando wachifumu panali chifaniziro ngati maonekedwe ake a munthu wokhala pamwamba pake.


Ngati maonekedwe a utawaleza uli m'mtambo tsiku la mvula, momwemo maonekedwe a kunyezimira kwake pozungulira pake. Ndiwo maonekedwe a chifaniziro cha ulemerero wa Yehova. Ndipo pakuchipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mau a wina wakunena.


Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kuthambo lokhala pamwamba pa mitu ya akerubi kudaoneka ngati mwala wasafiro, ngati maonekedwe a chifaniziro cha mpando wachifumu pamwamba pao.


Unali mu Edeni, munda wa Mulungu, mwala uliwonse wa mtengo wake unali chofunda chako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golide; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu.


Ndipo ndinaona mngelo wina wolimba alikutsika Kumwamba, wovala mtambo; ndi utawaleza pamutu pake, ndi nkhope yake ngati dzuwa, ndi mapazi ake ngati mizati yamoto;


ndipo unakhala nao ulemerero wa Mulungu; kuunika kwake kunafanana ndi mwala wa mtengo wake woposa, ngati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati krustalo;