Ndipo anamva mau a Yehova Mulungu alinkuyendayenda m'munda nthawi yamadzulo: ndipo anabisala Adamu ndi mkazi wake pamaso pa Yehova Mulungu pakati pamitengo ya m'munda.
Amosi 9:3 - Buku Lopatulika Angakhale abisala pamwamba pa Karimele, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Angakhale abisala pamwamba pa Karimele, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngakhale akabisale pamwamba pa phiri la Karimele, ndidzaŵaunguza nkuŵagwira. Ngakhale akabisale pansi pa nyanja yaikulu, ndidzalamula chilombo cham'nyanjamo kuti chiŵalume. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale atakabisala pamwamba pa phiri la Karimeli, Ine ndidzawasaka kumeneko ndi kuwagwira. Ngakhale atakabisala pansi pa nyanja yayikulu, ndidzalamula njoka kuti iwalume kumeneko. |
Ndipo anamva mau a Yehova Mulungu alinkuyendayenda m'munda nthawi yamadzulo: ndipo anabisala Adamu ndi mkazi wake pamaso pa Yehova Mulungu pakati pamitengo ya m'munda.
Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga Leviyatani njoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching'ona chimene chili m'nyanja.
Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pake ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe.
Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali mu Ziyoni, nadzamveketsa mau ake ali mu Yerusalemu; podyetsa abusa padzachita chisoni, ndi mutu wa Karimele udzauma.