Masiku ambiri tsono Israele anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda chilamulo;
Amosi 8:11 - Buku Lopatulika Taonani, akudza masiku, ati Ambuye Yehova, akuti ndidzatumiza njala m'dzikomo, si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mau a Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Taonani, akudza masiku, ati Ambuye Yehova, akuti ndidzatumiza njala m'dzikomo, si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mau a Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ambuye Chauta akunena kuti, “Nthaŵi ikubwera pamene ndidzagwetsa njala m'dzikomo. Siidzakhala njala ya buledi, kapena ludzu la madzi ai, koma njala yosoŵa mau a Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Nthawi ikubwera,” Ambuye Yehova akunena kuti, “Ndidzagwetsa njala mʼdziko lonse; osati njala ya chakudya kapena ludzu la madzi, koma njala yofuna kumva mawu a Yehova. |
Masiku ambiri tsono Israele anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda chilamulo;
Sitiziona zizindikiro zathu; palibenso mneneri; ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti.
ndipo ndidzaupasula; sudzadzomboleredwa kapena kulimidwa; koma padzamera lunguzi ndi minga; ndidzalamuliranso mitambo kuti isavumbwepo mvula.
Lidzafika tsoka lotsatanatsatana, kudzakhalanso mbiri yotsatanatsatana, ndipo adzafunafuna masomphenya a mneneri, koma malamulo adzatayikira wansembe, uphungu ndi kutayikira akulu.
ndingamvule wamaliseche, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati chipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu;
chifukwa chake kudzakhala ngati usiku kwa inu, wopanda masomphenya; ndipo kudzadera inu, wopanda kulosa; ndi dzuwa lidzalowera aneneri, ndi usana udzawadera bii.
Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.
Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita.
Ndipo pamene Saulo anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankhe ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri.
Ndipo mwanayo Samuele anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzikamodzi; masomphenya sanaonekeoneke.