Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Amosi 8:1 - Buku Lopatulika

Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, dengu la zipatso zamalimwe.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, dengu la zipatso zamalimwe.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zinanso zimene Ambuye Chauta adandiwonetsa m'masomphenya ndi izi: Panali dengu la zipatso zakupsa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: dengu la zipatso zakupsa.

Onani mutuwo



Amosi 8:1
6 Mawu Ofanana  

Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am'nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babiloni.


Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, anaumba dzombe, poyamba kuphuka kwa udzu wa chibwereza; ndipo taonani, ndicho chibwereza atawusengera mfumu.


chifukwa chake atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m'mzinda, ndi ana ako aamuna ndi aakazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa chingwe, ndi iwe mwini udzafa m'dziko lodetsedwa; ndipo Israele adzatengedwadi ndende kuchoka m'dziko lake.


Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye Yehova anaitana kuti atsutse ndi moto; ndipo unanyambita chakuya chachikulu ukadanyambitanso dziko.


Anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye anaima pa khoma lomangidwa ndi chingwe cholungamitsira chilili; ndi chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja lake.


Ndipo anati, Amosi uona chiyani? Ndipo ndinati, Dengu la zipatso zamalimwe. Nati Yehova kwa ine, Chitsiriziro chafikira anthu anga Israele, sindidzawalekanso.