Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga padziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga izo.
Amosi 7:6 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anachileka. Ichi chomwe sichidzachitika, ati Ambuye Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anachileka. Ichi chomwe sichidzachitika, ati Ambuye Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Chauta adakhululuka, ndipo adati, “Zimenezinso sizidzachitika konse.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero Yehova anakhululuka. Ambuye Yehova anati, “Izinso sizidzachitika.” |
Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga padziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga izo.
Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka choipachi; nati kwa mthenga wakuononga, Chakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi.
Koma Iye pokhala ngwa chifundo, anakhululukira choipa, osawaononga; nabweza mkwiyo wake kawirikawiri, sanautse ukali wake wonse.
Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi Yuda wonse anamupha iye konse? Kodi sanamuope Yehova, napembedzera Yehova, ndipo Yehova analeka choipa chimene ananenera iwo? Chotero tidzaichitira miyoyo yathu choipa chachikulu.
Ngati mudzakhalabe m'dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa nacho chisoni choipa chimene ndakuchitirani inu.
ndipo ng'ambani mitima yanu, si zovala zanu ai; ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wachisomo, ndi wodzala chifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wochuluka kukoma mtima, ndi woleka choipacho.
Anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye anaima pa khoma lomangidwa ndi chingwe cholungamitsira chilili; ndi chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja lake.
Ndipo Mulungu anaona ntchito zao, kuti anabwera kuleka njira yao yoipa; ndipo Mulungu analeka choipa adanenachi kuti adzawachitira, osachichita.
Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.
Pamenepo anachotsa milungu yachilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wake unagwidwa chisoni chifukwa cha mavuto a Israele.
Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m'dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa chisoni pa kubuula kwao chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.