Amosi 7:5 - Buku Lopatulika Pamenepo ndinati, Ambuye Yehova, lekanitu; Yakobo adzakhala chilili bwanji? Pakuti ali wamng'ono. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo ndinati, Ambuye Yehova, lekanitu; Yakobo adzakhala chilili bwanji? Pakuti ali wamng'ono. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ine ndidati, “Inu Ambuye Chauta, ndapota nanu, basi lekani. Kodi anthu a Yakobeŵa angalimbike bwanji? Iwoŵa ndi ofooka kwambiri.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, chonde ndikukupemphani, lekani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!” |
Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang'onong'ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora.
Ndipo padzatuluka pa izo mayamikiro ndi mau a iwo okondwerera; ndipo ndidzachulukitsa iwo, sadzakhala owerengeka; ndidzawachitiranso ulemu, sadzachepa.
Ndipo kunali, alimkukantha iwo, nditatsala ine, ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kufuula, ndi kuti, Kalanga ine, Ambuye Mulungu! Kodi mudzaononga otsala onse a Israele pakutsanulira ukali wanu pa Yerusalemu?
Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao?
Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? Pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse.
Khululukiranitu mphulupulu ya anthu awa, monga mwa chifundo chanu chachikulu, ndi monga mudalekerera anthu awa, kuyambira Ejipito kufikira tsopano.