Ndipo zofunkha zanu zidzasonkhanitsidwa, monga ziwala zisonkhana; monga dzombe atumpha, iwo adzatumpha pa izo.
Amosi 7:1 - Buku Lopatulika Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, anaumba dzombe, poyamba kuphuka kwa udzu wa chibwereza; ndipo taonani, ndicho chibwereza atawusengera mfumu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, anaumba dzombe, poyamba kuphuka kwa udzu a chibwereza; ndipo taonani, ndicho chibwereza atawasengera mfumu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Izi ndizo zimene Ambuye Chauta adandiwonetsa m'masomphenya: Chauta ankapanga dzombe pa nthaŵi yoti mfumu inali itamweta kale udzu, ndipo udzuwo unkaphukanso kachiŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Yehova ankasonkhanitsa gulu la dzombe nthawi imene gawo la zokolola za mfumu linali litakololedwa kale ndipo mbewu zachiwiri zinali zitangoyamba kumera kumene. |
Ndipo zofunkha zanu zidzasonkhanitsidwa, monga ziwala zisonkhana; monga dzombe atumpha, iwo adzatumpha pa izo.
Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am'nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babiloni.
Chosiya chimbalanga, dzombe lidachidya; ndi chosiya dzombe, chirimamine adachidya; ndi chosiya chirimamine, anoni adachidya.
Ndipo ndidzakubwezerani zaka zidazidya dzombe, ndi chirimamine, ndi anoni, ndi chimbalanga, gulu langa lalikulu la nkhondo, limene ndinalitumiza pakati pa inu.
Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni; minda yanu yochuluka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi ya azitona, yaonongeka ndi dzombe; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.
Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye Yehova anaitana kuti atsutse ndi moto; ndipo unanyambita chakuya chachikulu ukadanyambitanso dziko.
Anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye anaima pa khoma lomangidwa ndi chingwe cholungamitsira chilili; ndi chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja lake.
Ndipo ndidzadzudzula zolusa chifukwa cha inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zake, zosacha m'munda, ati Yehova wa makamu.