Kuti ng'ombe zathu zikhale zosenza katundu; ndi kuti pasakhale kupasula linga kapena kutulukamo, pasakhalenso kufuula m'makwalala athu.
Amosi 5:3 - Buku Lopatulika Pakuti atero Ambuye Yehova, M'nyumba ya Israele, mzinda wotulukamo chikwi chimodzi adzautsalira zana limodzi, ndi uwu wotulukamo zana limodzi adzautsalira khumi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti atero Ambuye Yehova, M'nyumba ya Israele, mudzi wotulukamo chikwi chimodzi adzautsalira zana limodzi, ndi uwu wotulukamo zana limodzi adzautsalira khumi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi: “Mzinda umene udapita ku nkhondo ndi anthu chikwi udzatsala ndi anthu zana limodzi chabe. Ndipo umene udapita ku nkhondo ndi anthu zana limodzi, udzatsala ndi anthu khumi okha a m'banja la Israele.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ambuye Yehova akuti, “Mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 1,000 amphamvu udzatsala ndi anthu 100 okha; mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 100 amphamvu udzatsala ndi anthu khumi okha basi.” |
Kuti ng'ombe zathu zikhale zosenza katundu; ndi kuti pasakhale kupasula linga kapena kutulukamo, pasakhalenso kufuula m'makwalala athu.
Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang'onong'ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora.
Popeza ngakhale anthu anu Israele akunga mchenga wa kunyanja, otsala ao okhaokha adzabwera; chionongeko chatsimikizidwa chilungamo chake chisefukira.
Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m'menemo, lidzadyedwanso; monga kachere, ndi monganso thundu, imene tsinde lake likhalabe ataigwetsa; chotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lake.
Koma ndidzawasiya owerengeka apulumuke lupanga, ndi njala, ndi mliri, kuti afotokoze zonyansa zao kwa amitundu kumene afikako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Ndipo Yesaya afuula za Israele, kuti, Ungakhale unyinji wa ana a Israele ukhala monga mchenga wa kunyanja, chotsalira ndicho chidzapulumuka.
Ndipo mudzatsala anthu pang'ono, mungakhale mudachuluka ngati nyenyezi za m'mwamba; popeza simunamvere mau a Yehova Mulungu wanu.
Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.
Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang'ono mwa amitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao.