Nthunthumirani, inu akazi, amene mulinkukhala phee; vutidwani, inu osasamalira, vulani mukhale maliseche, nimumange chiguduli m'chuuno mwanu.
Amosi 4:12 - Buku Lopatulika Chifukwa chake ndidzatero nawe, Israele; popeza ndidzakuchitira ichi, dzikonzeretu kukomana ndi Mulungu wako, Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake ndidzatero nawe, Israele; popeza ndidzakuchitira ichi, dzikonzeretu kukomana ndi Mulungu wako, Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Tsono inu Aisraele ndidzakuteroni. Ndipo chifukwa choti ndidzakuchitani zimenezi, inu Aisraele, konzekani kuti mukumane ndi Mulungu wanu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Choncho izi ndi zimene ndidzakuchitire iwe Israeli, chifukwa ndidzakuchitira zimenezi, konzekera kukumana ndi Mulungu wako, iwe Israeli.” |
Nthunthumirani, inu akazi, amene mulinkukhala phee; vutidwani, inu osasamalira, vulani mukhale maliseche, nimumange chiguduli m'chuuno mwanu.
Maliseche ako adzakhala osafundidwa, inde, manyazi ako adzaoneka; ndidzachita kubwezera, osasamalira munthu.
monga pamene moto uyatsa zitsamba, ndi moto uwiritsa madzi; kudziwitsa kwa amaliwongo anu dzina lanu, kuti amitundu anthunthumire pamaso panu.
Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.
Simunakwera kuima mopasuka, kapena kumanganso linga la nyumba ya Israele, kuima kunkhondo tsiku la Yehova.
Ndipo ndinafunafuna munthu pakati pao wakumanganso linga, ndi kuimira dziko popasukira pamaso panga, kuti ndisaliononge; koma ndinapeza palibe.
Ndidzakomana nao ngati chimbalangondo chochilanda ana ake, ndi kung'amba chokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; chilombo chidzawamwetula.
Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yake, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wake;
Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthawi m'mene simuganizira, Mwana wa Munthu adzadza.
Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, nuponyedwe iwe m'nyumba yandende.
Chifukwa chake kumbukira umo unalandira nunamvamo; nusunge nulape. Ukapanda kudikira tsono, ndidzafika ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yake ndidzadza pa iwe.