Amosi 3:7 - Buku Lopatulika Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zoonadi, Ambuye Chauta sachita kanthu osadziŵitsa atumiki ao, aneneri, zimene akonzekera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zoonadi Ambuye Yehova sachita kanthu asanawulule zimene akufuna kuchita kwa atumiki ake, aneneri. |
Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.
Mukani, funsirani ine, ndi anthu, ndi Yuda yense, kwa Yehova za mau a buku ili adalipeza; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukulu; popeza atate athu sanamvere mau a buku ili, kuchita monga mwa zonse zotilemberamo.
Chifukwa chake, taona, ndidzakusonkhanitsa ukhale ndi makolo ako, nudzatengedwa ulowe m'manda mwako mumtendere; ndipo sudzaona m'maso mwako choipa chonse ndidzachifikitsira malo ano. Ndipo anambwezera mfumu mau.
Nati mmodzi wa anyamata ake, Iai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israele ndiye amafotokozera mfumu ya Israele mau muwanena m'kati mwake mwa chipinda chanu chogonamo.
Pakuti Yehova watero kwa ine, Ine ndidzakhala chete, ndipo ndidzayang'ana mokhala chete, ndipo ndidzayang'ana mokhalamo Ine, monga kuwala kotentha kwa dzuwa, monga mtambo wa mame m'kutentha kwa masika.
Koma akadaima mu upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo kunjira yao yoipa, ndi kuchoipa cha ntchito zao.
Tsiku ilo ndidzameretsera nyumba ya Israele nyanga; ndipo ndidzakutsegulira pakamwa pakati pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Koma ndidzakufotokozera cholembedwa pa lemba la choonadi; ndipo palibe wina wakudzilimbikitsa pamodzi ndi ine, kutsutsana ndi aja, koma Mikaele kalonga wanu.
Ndipo tsopano ndikufotokozera choonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu mu Persiya, ndi yachinai idzakhala yolemera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwake idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Agriki.
Mfumu inamyankha Daniele, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wovumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kuvumbulutsa chinsinsi ichi.
Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.
Chivumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane;
Chifukwa chake lemba zimene unaziona, ndi zimene zilipo, ndi zimene zidzaoneka m'tsogolomo;
komatu m'masiku a mau a mngelo wachisanu ndi chiwiri m'mene iye adzayamba kuomba lipenga, pamenepo padzatsirizika chinsinsi cha Mulungu, monga analalikira kwa akapolo ake aneneri.
Zitatha izi ndinapenya, ndipo taonani, khomo lotseguka mu Mwamba, ndipo mau oyamba ndinawamva, ngati lipenga lakulankhula ndi ine, anati, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kuchitika m'tsogolomo.
Ndipo Yehova anaululiratu m'khutu la Samuele dzulo lake la tsiku limene Saulo anabwera, kuti,