Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.
Amosi 3:5 - Buku Lopatulika Kodi mbalame idzakodwa mumsampha pansi popanda msampha woitchera? Kodi msampha ufwamphuka pansi wosakola kanthu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi mbalame idzakodwa mumsampha pansi popanda msampha woitchera? Kodi msampha ufwamphuka pansi wosakola kanthu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi mbalame nkukatera pa msampha pansi, popanda nyambo yake? Nanga msamphawo kodi nkufwamphuka pansipo, usanakole kanthu? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi mbalame nʼkutera pa msampha pamene palibe nyambo yake? Kodi msampha umafwamphuka usanakole kanthu? |
Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.
Pakuti munthu sadziwatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa mu ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.
Ndipo padzakhala kuti, monga ndayang'anira iwo kuzula ndi kupasula ndi kugwetsa, ndi kuononga ndi kusautsa; momwemo ndidzayang'anira iwo kumangitsa mudzi ndi kubzala, ati Yehova.
Chifukwa chake Yehova wakhala maso pa choipacho, ndi kutifikitsira icho; pakuti Yehova Mulungu wathu ali wolungama mu ntchito zake zonse azichita; ndipo sitinamvere mau ake.
Kodi mkango udzabangula m'nkhalango wosakhala nayo nyama? Kodi msona wa mkango udzalira m'ngaka mwake usanagwire kanthu?
Kodi adzaomba lipenga m'mzinda osanjenjemera anthu? Kodi choipa chidzagwera mzinda osachichita Yehova?