Ndipo ana aamuna a Yakobo anadza kwa ophedwa nafunkha mzinda chifukwa anamuipitsa mlongo wao.
Amosi 3:11 - Buku Lopatulika Chifukwa chake, atero Ambuye Yehova, Padzakhala mdani pozungulira pake padziko, nadzatsitsa kukuchotsera mphamvu yako; ndi za m'nyumba zako zachifumu adzazifunkha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake, atero Ambuye Yehova, Padzakhala mdani pozungulira pake pa dziko, nadzatsitsa kukuchotsera mphamvu yako; ndi za m'nyumba zako zachifumu adzazifunkha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake Ambuye Chauta mau ao ndi aŵa: “Adani adzalizinga dzikolo, malinga ake adzaŵagwetsa, ndipo adzafunkha zonse zam'menemo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akunena izi: “Mdani adzalizungulira dzikoli; iye adzagwetsa malinga ako, ndi kufunkha nyumba zako zaufumu.” |
Ndipo ana aamuna a Yakobo anadza kwa ophedwa nafunkha mzinda chifukwa anamuipitsa mlongo wao.
Pamenepo Pulo mfumu ya Asiriya anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Pulo matalente a siliva chikwi chimodzi; kuti dzanja lake likhale naye kukhazikitsa ufumu m'dzanja lake.
Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.
Ndipo anatentha nyumba ya Mulungu, nagumula linga la Yerusalemu, natentha nyumba zake zonse zachifumu ndi moto, naononga zipangizo zake zonse zokoma.
Pakuti sadziwa kuchita zolungama, amene akundika zachiwawa ndi umbala m'nyumba zao zachifumu, ati Yehova.
Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yachisanu, pamodzi ndi nyumba ya nyengo yadzuwa; ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuluzo zidzatha, ati Yehova.
Pakuti taonani, ndidzakuutsirani mtundu wa anthu, nyumba ya Israele, ati Yehova Mulungu wa makamu; ndipo adzakupsinjani kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa kuchidikha.
Ambuye Yehova walumbira pali Iye mwini, ati Yehova Mulungu wa makamu, Ndinyansidwa nako kudzikuza kwa Yakobo, ndidana nazo nyumba zake zachifumu; m'mwemo ndidzapereka mzinda, ndi zonse zili m'menemo.