Olimba mtima chifunkhidwa chuma chao, agona tulo tao; amuna onse amphamvu asowa manja ao.
Amosi 2:16 - Buku Lopatulika ndi wolimba mtima mwa ngwazi adzathawa wamaliseche tsiku lomwelo, ati Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi wolimba mtima mwa ngwazi adzathawa wamaliseche tsiku lomwelo, ati Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku limenelo ngakhale wolimba mtima pakati pa anthu a mphamvu, adzathaŵa ali maliseche.” Akuterotu Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale asilikali olimba mtima kwambiri adzathawa ali maliseche pa tsikulo,” akutero Yehova. |
Olimba mtima chifunkhidwa chuma chao, agona tulo tao; amuna onse amphamvu asowa manja ao.
Keriyoti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Mowabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.
Koma Sisera anathawira choyenda pansi ku hema wa Yaele mkazi wa Hebere Mkeni; pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori, ndi nyumba ya Hebere Mkeni.