Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Mowabu, ndi a kuphiri la Seiri, amene simunalole Israele awalowere, pakutuluka iwo m'dziko la Ejipito, koma anawapatukira osawaononga;
Amosi 1:11 - Buku Lopatulika Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinani, sindidzabweza kulanga kwake; popeza analondola mphwake ndi lupanga, nafetsa chifundo chake chonse, ndi mkwiyo wake unang'amba ching'ambire nasunga mkwiyo wake chisungire; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinani, sindidzabweza kulanga kwake; popeza analondola mphwake ndi lupanga, nafetsa chifundo chake chonse, ndi mkwiyo wake unang'amba ching'ambire nasunga mkwiyo wake chisungire; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Edomu akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo adathamangitsa abale ao lupanga lili kumanja, popanda nchifundo chomwe. Ndiponso anali ndi ukali wosatonthozeka, ndi mkwiyo wosapozeka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Edomu akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anathamangitsa mʼbale wake ndi lupanga, popanda nʼchifundo chomwe. Popeza mkwiyo wake unakulabe ndipo ukali wake sunatonthozeke, |
Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Mowabu, ndi a kuphiri la Seiri, amene simunalole Israele awalowere, pakutuluka iwo m'dziko la Ejipito, koma anawapatukira osawaononga;
tapenyani, m'mene atibwezera, kudzatiinga m'cholowa chanu, chimene munatipatsa chikhale cholowa chathu.
Yehova, kumbukirani ana a Edomu tsiku la Yerusalemu; amene adati, Gamulani, gamulani, kufikira maziko ake.
Pakuti sindidzatsutsana kunthawi zonse, sindidzakwiya masiku onse; pakuti mzimu udzalefuka pamaso pa Ine, ndi miyoyo imene ndinailenga.
Ejipito adzasanduka bwinja, ndi Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu, chifukwa cha chiwawachi anawachitira ana a Yuda; popeza anakhetsa mwazi wosachimwa m'dziko lao.
Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.
Ndipo ndikwiya nao amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang'ono, ndipo anathandizira choipa.
Ndakukondani, ati Yehova; koma inu mukuti, Mwatikonda motani? Esau si mkulu wake wa Yakobo kodi? Ati Yehova; ndipo ndinakonda Yakobo;
Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.
Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m'dziko lake.