Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.
Akolose 4:18 - Buku Lopatulika Ndipereka moni ndi dzanja langa, kwa ine Paulo. Kumbukirani zomangira zanga. Chisomo chikhale nanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipereka moni ndi dzanja langa, kwa ine Paulo. Kumbukirani zomangira zanga. Chisomo chikhale nanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndi dzanja langalanga ndikulemba mau aŵa: “Moni. Ndine Paulo.” Kumbukirani kuti ndili m'maunyolo. Mulungu akukomereni mtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa moni uwu. Kumbukirani kuti ndili mu unyolo. Chisomo chikhale ndi inu. |
Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.
Gayo, mwini nyumba wolandira ine, ndi Mpingo wonse wa Ambuye, akupereka moni. Erasto, ndiye woyang'anira mzinda, akupereka moni, ndiponso Kwarto mbaleyo.
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.
monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.
ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende,
Ndipereka moni ndi dzanja langa Paulo; ndicho chizindikiro m'kalata aliyense; ndiko kulemba kwanga.
Potero usachite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wake; komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu;
Akukupatsa moni onse akukhala pamodzi ndi ine. Pereka moni kwa otikondawo m'chikhulupiriro. Chisomo chikhale ndi inu nonse.
Kumbukirani am'nsinga, monga am'nsinga anzao; ochitidwa zoipa, monga ngati inunso adatero nanu m'thupi.