ndipo mupereke moni kwa Mpingo wa Ambuye wa m'nyumba mwao. Moni kwa Epeneto wokondedwa wanga, ndiye chipatso choyamba cha Asiya cha kwa Khristu.
Akolose 4:15 - Buku Lopatulika Perekani moni kwa abalewo a mu Laodikea, ndi Nimfa, ndi Mpingowo wa m'nyumba yao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akupatsani moni abalewo a m'Laodikea, ndi Nimfa, ndi Mpingowo wa m'nyumba yao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mutiperekereko moni kwa abale athu okhala ku Laodikea, ndiponso kwa Nimfa ndi kwa ampingo amene amasonkhana kunyumba kwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Perekani moni kwa abale a ku Laodikaya, ndiponso kwa Numfa ndi mpingo wa mʼnyumba mwake. |
ndipo mupereke moni kwa Mpingo wa Ambuye wa m'nyumba mwao. Moni kwa Epeneto wokondedwa wanga, ndiye chipatso choyamba cha Asiya cha kwa Khristu.
Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.
Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndili nayo chifukwa cha inu, ndi iwowa a mu Laodikea, ndi onse amene sanaone nkhope yanga m'thupi;
Pakuti ndimchitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo ntchito chifukwa cha inu, ndi iwo a mu Laodikea, ndi iwo a mu Hierapoli.
Ndipo pamene mudamwerenga kalata iyi, amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikea, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikea.
ndi kwa Afiya mlongoyo, ndi Arkipo msilikali mnzathu, ndi kwa Mpingo uli m'nyumba yako: