Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.
Akolose 4:13 - Buku Lopatulika Pakuti ndimchitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo ntchito chifukwa cha inu, ndi iwo a mu Laodikea, ndi iwo a mu Hierapoli. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ndimchitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo ntchito chifukwa cha inu, ndi iwo a m'Laodikea, ndi iwo a m'Hierapoli. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndingathe kumchitira umboni kuti amagwira ntchito kwambiri chifukwa cha inu, ndiponso chifukwa cha anthu okhala ku Laodikea ndi ku Hierapoli. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndikumuchitira umboni kuti amagwira ntchito mwamphamvu chifukwa cha inu ndiponso kwa amene ali ku Laodikaya ndi Herapoli. |
Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.
Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndili nayo chifukwa cha inu, ndi iwowa a mu Laodikea, ndi onse amene sanaone nkhope yanga m'thupi;
ndi kuti, Chimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smirina, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiatira, ndi ku Sardi, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikea.